-
Genesis 13:10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Choncho, Loti anakweza maso ake n’kuona Chigawo* chonse cha Yorodano+ mpaka kukafika ku Zowari,+ ndipo anaona kuti chinali chigawo chobiriwira bwino. Chinali chobiriwira bwino kwambiri ngati mmene unalili munda wa Yehova+ komanso ngati mmene linalili dziko la Iguputo. Pa nthawiyi n’kuti Yehova asanawononge Sodomu ndi Gomora.
-
-
Ezekieli 31:8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Mitengo ina ya mkungudza sinafanane ndi mtengo umenewu m’munda wa Mulungu.+ Nthambi zikuluzikulu za mitengo ina yooneka ngati mkungudza, sizinafanane ndi za mtengo umenewu. Nthambi za mitengo ya katungulume sizinafanane ndi nthambi za mtengo umenewu. Panalibenso mtengo wina m’munda wa Mulungu umene unali wokongola ngati mtengo umenewu.+
-