Levitiko 5:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 “‘Munthu akakhudza chinthu chodetsedwa, kaya ikhale nyama yakufa yakuthengo, nyama yakufa yoweta, kapena kamodzi mwa tizilombo topezeka tambiri,+ ngakhale kuti sanazindikire zotsatira zake,+ iye ndi wodetsedwa ndipo wapalamula mlandu.+ Ezekieli 44:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 “‘Iwo aziphunzitsa anthu anga za kusiyana kwa chinthu chopatulika ndi chinthu choipitsidwa. Aziwaphunzitsa kuti adziwe kusiyana kwa chinthu chodetsedwa ndi choyera.+ Hagai 2:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Ndiyeno Hagai anafunsanso kuti: “Ngati munthu amene wadetsedwa chifukwa chokhudza mtembo atakhudza chilichonse mwa zinthu zimenezi, kodi chingakhale chodetsedwa?”+ Ansembewo anayankha kuti: “Inde, chingakhale chodetsedwa.” Aefeso 5:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 ndipo musamachite nawo+ ntchito zosapindulitsa za mu mdima.+ M’malomwake, muzidzudzula ntchitozo.+
2 “‘Munthu akakhudza chinthu chodetsedwa, kaya ikhale nyama yakufa yakuthengo, nyama yakufa yoweta, kapena kamodzi mwa tizilombo topezeka tambiri,+ ngakhale kuti sanazindikire zotsatira zake,+ iye ndi wodetsedwa ndipo wapalamula mlandu.+
23 “‘Iwo aziphunzitsa anthu anga za kusiyana kwa chinthu chopatulika ndi chinthu choipitsidwa. Aziwaphunzitsa kuti adziwe kusiyana kwa chinthu chodetsedwa ndi choyera.+
13 Ndiyeno Hagai anafunsanso kuti: “Ngati munthu amene wadetsedwa chifukwa chokhudza mtembo atakhudza chilichonse mwa zinthu zimenezi, kodi chingakhale chodetsedwa?”+ Ansembewo anayankha kuti: “Inde, chingakhale chodetsedwa.”
11 ndipo musamachite nawo+ ntchito zosapindulitsa za mu mdima.+ M’malomwake, muzidzudzula ntchitozo.+