21 Ndipo munthu akakhudza chodetsa chilichonse, kaya chodetsa cha munthu+ kapena nyama yodetsedwa,+ kapenanso chinthu chilichonse chonyansa chodetsedwa,+ n’kudyako nyama ya nsembe yachiyanjano, imene ndi ya Yehova, munthu wotero aziphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake.’”