13 Ndipo Aisiraeli onse akamulira+ ndi kumuika m’manda. Iwo akamulira popeza m’banja lonse la Yerobowamu, uyu yekha ndiye adzaikidwe m’manda chifukwa chakuti Yehova Mulungu wa Isiraeli, wapeza chinachake chabwino mwa yekhayu m’nyumba yonse ya Yerobowamu.+