11 “Mitundu yambiri ya anthu idzadziphatika kwa Yehova pa tsikulo,+ choncho adzakhala anthu anga.+ Ine ndidzakhala mwa iwe.” Ndipo udzadziwa kuti Yehova wa makamu wandituma kwa iwe.+
10 Pakuti kale simunali mtundu, koma tsopano ndinu mtundu wa anthu a Mulungu.+ Munali anthu amene sanakuchitireni chifundo, koma tsopano ndinu amene mwachitiridwa chifundo.+