17 Anthu amene akudzipatula ndi kudziyeretsa kuti apite kuminda+ n’kukaima kuseri kwa fano limene lili pakati pa mundawo, amene akudya nyama ya nkhumba+ ndi chinthu chonyansa, amene akudya ngakhale makoswe,+ onsewo adzathera limodzi,” akutero Yehova.