Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 12:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Odalitsa iwe ndidzawadalitsa, ndipo otemberera iwe ndidzawatemberera.+ Mabanja onse a padziko lapansi adzapeza madalitso* chifukwa cha iwe.”+

  • Salimo 37:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Olungama adzalandira dziko lapansi,+

      Ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.+

  • Yesaya 49:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Yehova wanena kuti: “Pa nthawi yapadera yosonyeza kukoma mtima kwanga, ndinakuyankha.+ M’tsiku la chipulumutso, ndinakuthandiza.+ Ndinakuteteza kuti ndikupereke ngati pangano kwa anthu,+ kuti ndikonzenso dzikolo,+ kuti anthu ayambirenso kukhala m’cholowa chawo chimene chinali bwinja,+

  • Mateyu 25:34
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 34 “Pamenepo mfumu idzauza a kudzanja lake lamanja kuti, ‘Bwerani, inu amene mwadalitsidwa ndi Atate+ wanga. Lowani+ mu ufumu+ umene anakonzera inu kuchokera pa kukhazikitsidwa kwa dziko.+

  • Yohane 10:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 “Ndili ndi nkhosa zina+ zimene sizili za khola ili,+ zimenezonso ndiyenera kuzibweretsa. Zidzamva mawu anga,+ ndipo zidzakhala gulu limodzi ndi m’busa mmodzi.+

  • 2 Petulo 3:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Koma pali kumwamba kwatsopano+ ndi dziko lapansi latsopano+ zimene ife tikuyembekezera mogwirizana ndi lonjezo lake, ndipo mmenemo mudzakhala chilungamo.+

  • Chivumbulutso 7:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Zimenezi zitatha, nditayang’ana ndinaona khamu lalikulu la anthu,+ limene palibe munthu aliyense amene anatha kuliwerenga, lochokera m’dziko lililonse,+ fuko lililonse, mtundu uliwonse,+ ndi chinenero chilichonse.+ Iwo anali ataimirira pamaso pa mpando wachifumu+ ndi pamaso pa Mwanawankhosa, atavala mikanjo yoyera+ ndiponso atanyamula nthambi za kanjedza+ m’manja mwawo.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena