Yesaya 10:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 M’tsiku limenelo, otsala a Isiraeli+ ndi opulumuka a nyumba ya Yakobo sadzadaliranso yemwe akuwamenya,+ koma ndi mtima wonse adzadalira Yehova, Woyera wa Isiraeli.+ Yeremiya 23:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Koma adzalumbira kuti, ‘Pali Yehova Mulungu wamoyo amene anatulutsa a m’nyumba ya Isiraeli ndi kuwabweretsa kuno kuchokera m’dziko la kumpoto komanso kuchokera m’mayiko onse kumene ndinawabalalitsira’ ndipo adzakhala m’dziko lawo.”+ Zekariya 8:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 ‘M’dzikolo mudzakhala mbewu ya mtendere.+ Mpesa udzabala zipatso+ ndipo dziko lapansi lidzapereka zokolola zake.+ Kumwamba kudzagwetsa mame ake.+ Ndidzachititsa kuti anthu otsala+ mwa anthu awa adzalandire zinthu zonsezi.+ Aroma 11:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 Mwa njira imeneyi, Aisiraeli onse+ adzapulumuka. Izi zikugwirizana ndi zimene Malemba amanena kuti: “Wolanditsa adzachokera m’Ziyoni+ ndi kuchotsera Yakobo zochita zonse zosalemekeza Mulungu.+ 1 Petulo 2:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Koma inu ndinu “fuko losankhidwa mwapadera, ansembe achifumu, mtundu woyera,+ anthu odzakhala chuma chapadera,+ kuti mulengeze makhalidwe abwino kwambiri”+ a amene anakuitanani kuchoka mu mdima kulowa m’kuwala kwake kodabwitsa.+
20 M’tsiku limenelo, otsala a Isiraeli+ ndi opulumuka a nyumba ya Yakobo sadzadaliranso yemwe akuwamenya,+ koma ndi mtima wonse adzadalira Yehova, Woyera wa Isiraeli.+
8 Koma adzalumbira kuti, ‘Pali Yehova Mulungu wamoyo amene anatulutsa a m’nyumba ya Isiraeli ndi kuwabweretsa kuno kuchokera m’dziko la kumpoto komanso kuchokera m’mayiko onse kumene ndinawabalalitsira’ ndipo adzakhala m’dziko lawo.”+
12 ‘M’dzikolo mudzakhala mbewu ya mtendere.+ Mpesa udzabala zipatso+ ndipo dziko lapansi lidzapereka zokolola zake.+ Kumwamba kudzagwetsa mame ake.+ Ndidzachititsa kuti anthu otsala+ mwa anthu awa adzalandire zinthu zonsezi.+
26 Mwa njira imeneyi, Aisiraeli onse+ adzapulumuka. Izi zikugwirizana ndi zimene Malemba amanena kuti: “Wolanditsa adzachokera m’Ziyoni+ ndi kuchotsera Yakobo zochita zonse zosalemekeza Mulungu.+
9 Koma inu ndinu “fuko losankhidwa mwapadera, ansembe achifumu, mtundu woyera,+ anthu odzakhala chuma chapadera,+ kuti mulengeze makhalidwe abwino kwambiri”+ a amene anakuitanani kuchoka mu mdima kulowa m’kuwala kwake kodabwitsa.+