13 Ndiyetu tipatseni amunawo,+ anthu opanda pakewo,+ amene ali mu Gibeya,+ kuti tiwaphe+ ndi kuchotsa choipachi mu Isiraeli.”+ Koma ana a Benjamini sanafune kumvera mawu a abale awo, ana a Isiraeli.+
9 “Inu ana a Isiraeli, mwakhala mukuchimwa kuyambira m’masiku a Gibeya+ ndipo anthu anapitirizabe kuchita machimo kumeneko. Nkhondo ya ku Gibeya yomenyana ndi anthu osalungama sinawawononge onse.+