Yesaya 6:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Pamenepo ndinafunsa kuti: “Mpaka liti, Yehova?”+ Iye anayankha kuti: “Mpaka mizinda yawo itawonongedwa n’kukhala bwinja, yopanda wokhalamo. Mpaka nyumba zawo zitakhala zopanda anthu okhalamo, ndiponso mpaka nthaka itawonongekeratu.+ Hoseya 10:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Pakati pa anthu a mtundu wanu pachitika chisokonezo+ ndipo mizinda yanu yonse yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri idzawonongedwa,+ ngati mmene Salimani anawonongera Beti-aribeli. Iye anachita zimenezi pa tsiku lankhondo, pamene amayi anaphwanyidwaphwanyidwa pamodzi ndi ana awo.+ Amosi 3:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 “Chotero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pali mdani amene wazungulira dziko lonse+ ndipo ameneyo adzakukhalitsa wopanda mphamvu ndipo adzafunkha nsanja zako zokhalamo.’+ Mika 5:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Ine ndidzagwetsa mizinda ya m’dziko lanu. Ndidzagumula malo anu onse amene ali ndi mipanda yolimba kwambiri.+ Mika 7:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Dzikoli lidzakhala bwinja chifukwa cha zochita za anthu okhala mmenemo ndi zotsatirapo za zochita zawozo.+
11 Pamenepo ndinafunsa kuti: “Mpaka liti, Yehova?”+ Iye anayankha kuti: “Mpaka mizinda yawo itawonongedwa n’kukhala bwinja, yopanda wokhalamo. Mpaka nyumba zawo zitakhala zopanda anthu okhalamo, ndiponso mpaka nthaka itawonongekeratu.+
14 Pakati pa anthu a mtundu wanu pachitika chisokonezo+ ndipo mizinda yanu yonse yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri idzawonongedwa,+ ngati mmene Salimani anawonongera Beti-aribeli. Iye anachita zimenezi pa tsiku lankhondo, pamene amayi anaphwanyidwaphwanyidwa pamodzi ndi ana awo.+
11 “Chotero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pali mdani amene wazungulira dziko lonse+ ndipo ameneyo adzakukhalitsa wopanda mphamvu ndipo adzafunkha nsanja zako zokhalamo.’+
11 Ine ndidzagwetsa mizinda ya m’dziko lanu. Ndidzagumula malo anu onse amene ali ndi mipanda yolimba kwambiri.+
13 Dzikoli lidzakhala bwinja chifukwa cha zochita za anthu okhala mmenemo ndi zotsatirapo za zochita zawozo.+