Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 32:35
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 35 Kubwezera ndi kwanga, chilangonso ndi changa.+

      Pa nthawi yoikidwiratu phazi lawo lidzaterereka poyenda,+

      Pakuti tsiku la tsoka lawo layandikira,+

      Ndipo zowagwera zikufika mofulumira.’+

  • Salimo 27:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  2 Anthu ochita zoipa atandiyandikira kuti adye mnofu wanga,+

      Popeza kuti iwo ndi ondiukira komanso adani anga,+

      Anapunthwa ndi kugwa.+

  • Yeremiya 15:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Inu Yehova mukudziwa bwino mavuto anga.+ Ndikumbukireni+ ndipo mutembenuke ndi kundiyang’ana kuti mubwezere anthu ondizunza.+ Musandichotsere moyo wanga chifukwa chakuti simupsa mtima mwamsanga.+ Onani chitonzo chimene chili pa ine chifukwa cha dzina lanu.+

  • Yeremiya 15:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 “Ndakuchititsa kukhala ngati mpanda wamkuwa wolimba kwambiri kwa anthu awa.+ Iwo adzamenyana nawe ndithu, koma sadzakugonjetsa,+ pakuti ine ndili ndi iwe kuti ndikupulumutse ndi kukulanditsa,”+ watero Yehova.

  • Yeremiya 17:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Anthu amene amandizunza achite manyazi+ koma musalole kuti ineyo ndichite manyazi.+ Anthuwo agwidwe ndi mantha aakulu koma musalole kuti ine ndigwidwe ndi mantha aakulu. Agwetsereni tsoka+ ndipo muwaphwanye kuwirikiza kawiri.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena