Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yeremiya 14:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Ndiyeno Yehova anandiyankha kuti: “Aneneriwo akulosera monama m’dzina langa.+ Ine sindinawatume, kuwalamula, kapena kulankhula nawo.+ Maulosi amene akukuuzaniwo anthu inu, ndiwo masomphenya onama, maula, mawu opanda pake+ ndi chinyengo cha mumtima mwawo.+

  • Yeremiya 23:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 “Ine sindinatumize aneneriwo, koma okha anathamanga. Ine sindinalankhule nawo, koma okha analosera.+

  • Yeremiya 28:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Pamenepo mneneri Yeremiya anauza mneneri Hananiya+ kuti: “Tamvera iwe Hananiya! Yehova sanakutume, koma iwe wachititsa anthuwa kukhulupirira zinthu zonama.+

  • Yeremiya 29:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Aneneri anu komanso anthu ochita zamaula amene ali pakati panu asakunyengeni+ ndipo musamvere anthu amene akufotokoza maloto awo amene alota.+

  • Ezekieli 13:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 “Iwo aona masomphenya abodza ndipo alosera zonama.+ Akunena kuti, ‘Yehova wanena kuti,’ pamene Yehova sanawatume, ndipo akuyembekeza kuti zimene anenazo zichitika.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena