Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yeremiya 14:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Ndiyeno Yehova anandiyankha kuti: “Aneneriwo akulosera monama m’dzina langa.+ Ine sindinawatume, kuwalamula, kapena kulankhula nawo.+ Maulosi amene akukuuzaniwo anthu inu, ndiwo masomphenya onama, maula, mawu opanda pake+ ndi chinyengo cha mumtima mwawo.+

  • Yeremiya 29:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Aneneri anu komanso anthu ochita zamaula amene ali pakati panu asakunyengeni+ ndipo musamvere anthu amene akufotokoza maloto awo amene alota.+

  • Maliro 2:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Aneneri ako aona masomphenya achabechabe ndi opanda pake+ onena za iwe.

      Iwo sanaulule zolakwa zako kuti akuteteze n’cholinga choti usatengedwe kupita ku ukapolo,+

      Koma anali kuona masomphenya achabechabe ndi osocheretsa+ onena za iwe.

  • 2 Petulo 2:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Komabe, pakati pa anthuwo panadzakhala aneneri onyenga. Momwemonso padzakhala aphunzitsi onyenga pakati panu.+ Amenewa adzabweretsa mwakachetechete timagulu tampatuko towononga ndipo adzakana ngakhale iye amene anawagula,+ n’kudzibweretsera chiwonongeko chofulumira.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena