Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yeremiya 2:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Ansembe sanafunse kuti, ‘Ali kuti Yehova?’+ Ndipo anthu ophunzitsa chilamulo sanandidziwe.+ Abusa nawonso anaphwanya malamulo anga,+ ndipo aneneri anali kulosera m’dzina la Baala+ ndi kutsatira milungu yopanda phindu.+

  • Yeremiya 5:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 “Iwo akana Yehova, ndipo akunena kuti, ‘Iye kulibe.+ Ndipo ife tsoka silidzatigwera. Sitidzaona lupanga lililonse kapena njala yaikulu.’+

  • Yeremiya 5:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Aneneri akulosera monama,+ ndipo ansembe akupondereza anthu ndi mphamvu zawo.+ Anthu anga nawonso akukonda zimenezi.+ Ndipo kodi anthu inu mudzachita chiyani pamapeto pake?”+

  • Yeremiya 23:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Yehova wa makamu wanena kuti: “Musamvere mawu a aneneri amene akulosera kwa anthu inu.+ Akukulimbikitsani kuchita zinthu zopanda pake.+ Iwo akulankhula masomphenya a mumtima mwawo+ osati ochokera m’kamwa mwa Yehova.+

  • Yeremiya 27:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Anthu inu musamvere mawu a aneneri amene akukuuzani kuti, ‘Simudzatumikira mfumu ya Babulo,’+ chifukwa zimene akulosera kwa inuzo ndi zonama.+

  • Yeremiya 29:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Pakuti ‘zimene akukuuzanizo akulosera m’dzina langa monama. Ine sindinawatume,’+ watero Yehova.”’”

  • Ezekieli 13:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 “Iwe mwana wa munthu, losera zokhudza aneneri a mu Isiraeli.+ Uuze amene akulosera zam’mutu mwawo+ kuti, ‘Mvetserani mawu a Yehova.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena