-
Genesis 49:1Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
49 Pambuyo pake, Yakobo anaitana ana ake n’kuwauza kuti: “Sonkhanani pamodzi kuti ndikuuzeni zimene zidzachitika kwa inu m’masiku am’tsogolo.
-
-
Ezekieli 38:8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 “‘“Pakapita masiku ambiri, ine ndidzatembenukira kwa iwe. Pakatha zaka zambiri, iwe udzapita kudziko+ la anthu amene anapulumutsidwa ku lupanga ndi kubwerera kwawo. Udzapita kudziko la anthu amene anasonkhanitsidwa pamodzi kuchokera ku mitundu ina ya anthu+ n’kukakhala kumapiri a ku Isiraeli. Dziko lawo linali kuwonongedwa nthawi zonse ndipo tsopano muli anthu amene anachokera m’mayiko a anthu a mitundu ina. Onsewo akukhala m’dzikoli mwabata.+
-