2Awa ndiwo anali anthu a m’chigawo*+ amene anatuluka mu ukapolo+ wa anthu omwe Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo anawatengera+ ku Babulo. Anthuwa anabwerera+ ku Yerusalemu ndi ku Yuda,+ aliyense kumzinda wakwawo.
7 Ndibwezeretsa anthu a mu Yuda ndi a mu Isiraeli amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina,+ ndipo ndiwalimbitsa kuti akhale ngati mmene analili poyamba.+