Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 30:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Yehova Mulungu wanu adzabweza kwawo anthu a mtundu wanu amene anagwidwa ndi kupita kudziko lina,+ ndipo adzakumverani chifundo+ n’kukusonkhanitsaninso pamodzi kuchokera pakati pa anthu onse kumene Yehova Mulungu wanu anakubalalitsirani.+

  • Salimo 14:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  7 Haa! Zikanakhala bwino m’Ziyoni mukanapezeka chipulumutso cha Isiraeli.+

      Yehova akadzasonkhanitsa ndi kubwezeretsa anthu ake amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina,+

      Yakobo adzasangalale, Isiraeli adzakondwere.+

  • Yeremiya 30:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Pakuti, “taona! masiku adzafika,” watero Yehova, “pamene ndidzasonkhanitsa Isiraeli ndi Yuda,+ anthu anga amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina,” watero Yehova. “Iwo ndidzawabwezeretsa kudziko limene ndinapatsa makolo awo ndipo adzalitenga kukhalanso lawo.”’”+

  • Yeremiya 32:44
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 44 “‘Anthu adzagula minda ndi ndalama ndipo padzakhala kulemberana zikalata za pangano+ pamaso pa mboni ndi kumata zikalatazo.+ Zimenezi zidzachitika m’dziko la Benjamini,+ m’madera ozungulira Yerusalemu,+ m’mizinda ya Yuda,+ m’mizinda ya m’madera amapiri, m’mizinda ya m’chigwa+ ndi m’mizinda ya kum’mwera.+ Zidzakhala choncho chifukwa chakuti ndidzabwezeretsa anthu ake amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina,’+ watero Yehova.”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena