8 Chotero ana a Isiraeli anauza Samueli kuti: “Usakhale chete, koma utipempherere kwa Yehova Mulungu kuti atithandize,+ kuti atipulumutse m’manja mwa Afilisiti.”
19 Zitatero, anthu onse anayamba kuuza Samueli kuti: “Pempherera+ atumiki ako kwa Yehova Mulungu wako, chifukwa sitikufuna kufa. Pakuti tawonjeza choipa china pa machimo athu onse, mwa kupempha kuti tikhale ndi mfumu.”