10 Ndidzachititsa mantha anthu ambiri a mitundu ina chifukwa cha iwe.+ Ndikadzawaloza ndi lupanga langa kumaso,+ mafumu awo adzanjenjemera ndi mantha. Kuyambira pa tsiku limene udzaphedwe, aliyense wa iwo azidzanjenjemera nthawi zonse chifukwa choopa kufa.’+