4 Mfumuyo ikadzauka,+ ufumu wake udzasweka ndipo udzagawanika ndi kutengedwa ndi mphepo zinayi+ zakumwamba,+ koma sudzapita kwa mbadwa zake+ ndipo maufumuwo sadzafanana ndi ufumu wake. Zimenezi zidzachitika chifukwa ufumu wake udzazulidwa ndi kuperekedwa kwa ena.