Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 21:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Tsopano taonani! Kukubwera magaleta ankhondo okokedwa ndi mahatchi awiriawiri, mutakwera amuna ankhondo.”+

      Kenako iye anayamba kufuula kuti: “Wagwa! Babulo wagwa!+ Zifaniziro zonse zogoba za milungu yake zaphwanyidwa ndipo zili pansi.”+

  • Yesaya 47:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Koma zinthu ziwiri izi zidzakugwera modzidzimutsa tsiku limodzi:+ Ana ako adzafa ndiponso udzakhala wamasiye. Zimenezi zidzakugwera ndithu,+ chifukwa cha zamatsenga zochuluka zimene wachita, chifukwa cha kuchuluka kwa mphamvu zako zamatsenga, ndiponso chifukwa chakuti wazichita kwambiri.+

  • 1 Atesalonika 5:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Pakuti inu eni mukudziwa bwino kuti tsiku la Yehova*+ lidzabwera ndendende ngati mbala usiku.+

  • Chivumbulutso 14:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Kenako mngelo wina wachiwiri anamutsatira, ndipo anati: “Wagwa! Babulo+ Wamkulu wagwa,+ amene anachititsa mitundu yonse ya anthu kumwako vinyo+ wa mkwiyo wake ndi wa dama* lake!”+

  • Chivumbulutso 18:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Iye anafuula ndi mawu amphamvu,+ akuti: “Wagwa! Babulo Wamkulu wagwa,+ ndipo wakhala malo okhala ziwanda, ndiponso obisalamo mpweya+ uliwonse wonyansa wotuluka m’kamwa, komanso obisalamo mbalame iliyonse yonyansa ndi yodedwa.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena