Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 13:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Babulo, amene ndi chokongoletsera maufumu,+ chinthu chokongola ndi chonyadira cha Akasidi,+ adzakhala ngati pamene Mulungu anagonjetsa Sodomu ndi Gomora.+

  • Yesaya 14:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 mudzanene mwambi uwu wotonza mfumu ya Babulo:

      “Uja ankagwiritsa ntchito anzakeyu wasiya ndithu! Wopondereza uja waleka ndithu!+

  • Yesaya 45:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 45 Ine Yehova ndalankhula kwa wodzozedwa wanga.+ Ndalankhula kwa Koresi amene ndamugwira dzanja lake lamanja+ kuti ndigonjetse mitundu ya anthu pamaso pake,+ kuti ndimasule m’chiuno mwa mafumu, kuti ndimutsegulire zitseko zokhala ziwiriziwiri, moti ngakhale zipata sizidzatsekedwa. Ndalankhula kuti:

  • Yeremiya 50:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Pakuti mtundu wina wabwera kudzamuukira kuchokera kumpoto.+ Umenewu ndi mtundu umene wasandutsa dziko lake kukhala chinthu chodabwitsa, moti m’dzikoli mulibe aliyense wokhalamo.+ Anthu ndiponso ziweto zathawa.+ Zonse zapita.”+

  • Yeremiya 51:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Babulo wagwa mwadzidzidzi moti wasweka.+ Mulireni mofuula anthu inu.+ M’patseni mafuta a basamu kuti muthetse ululu wake,+ mwina achira.”

  • Danieli 5:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 “PERESI,* ufumu wanu wagawanika ndipo waperekedwa kwa Amedi ndi Aperisiya.”+

  • Chivumbulutso 14:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Kenako mngelo wina wachiwiri anamutsatira, ndipo anati: “Wagwa! Babulo+ Wamkulu wagwa,+ amene anachititsa mitundu yonse ya anthu kumwako vinyo+ wa mkwiyo wake ndi wa dama* lake!”+

  • Chivumbulutso 18:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Iye anafuula ndi mawu amphamvu,+ akuti: “Wagwa! Babulo Wamkulu wagwa,+ ndipo wakhala malo okhala ziwanda, ndiponso obisalamo mpweya+ uliwonse wonyansa wotuluka m’kamwa, komanso obisalamo mbalame iliyonse yonyansa ndi yodedwa.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena