Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ezara 1:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 1 M’chaka choyamba cha Koresi+ mfumu ya Perisiya, Yehova analimbikitsa+ mtima wa Koresi mfumu ya Perisiya kuti mawu a Yehova kudzera mwa Yeremiya+ akwaniritsidwe. Pamenepo Koresiyo anatumiza mawu amene analengezedwa+ mu ufumu wake wonse. Mawuwo analembedwanso m’makalata,+ kuti:

  • Yesaya 21:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Pali masomphenya ochititsa mantha+ amene ndaona: Mtundu wochita chinyengo ukuchita zachinyengo, ndipo mtundu wolanda zinthu ukulanda zinthu.+ Pita ukachite nkhondo, iwe Elamu! Kazungulire mzindawo, iwe Mediya!+ Ndathetsa kuusa moyo* konse kumene mzindawo unachititsa.+

  • Yesaya 45:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 45 Ine Yehova ndalankhula kwa wodzozedwa wanga.+ Ndalankhula kwa Koresi amene ndamugwira dzanja lake lamanja+ kuti ndigonjetse mitundu ya anthu pamaso pake,+ kuti ndimasule m’chiuno mwa mafumu, kuti ndimutsegulire zitseko zokhala ziwiriziwiri, moti ngakhale zipata sizidzatsekedwa. Ndalankhula kuti:

  • Yeremiya 50:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Inetu ndikuutsira Babulo mpingo wa mitundu yamphamvu ndi kubweretsa mitunduyo kuchokera kudziko la kumpoto.+ Mitunduyo idzamuukira+ ndi kulanda dziko lake.+ Mauta awo ndi ofanana ndi mauta a munthu wamphamvu amene amapha ana ndipo mautawo sabwerera osachitapo kanthu.+

  • Danieli 6:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Choncho zinthu zinamuyendera bwino Danieli mu ufumu wa Dariyo+ ndiponso mu ufumu wa Koresi Mperisiya.+

  • Danieli 9:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 M’chaka choyamba cha Dariyo mwana wa Ahasiwero,+ wa mtundu wa Amedi,+ amene anaikidwa kukhala mfumu ya ufumu wa Akasidi,+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena