Yeremiya 51:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 “Nolani mivi yanu.+ Dzitetezeni ndi zishango zozungulira, amuna inu. Yehova wautsa mitima ya mafumu a Amedi,+ chifukwa akufuna kulanga Babulo ndi kumuwononga.+ Yehova akufuna kubwezera Babulo chilango chifukwa cha kachisi wake.+ Yeremiya 51:28 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 28 Konzekeretsani mitundu ya anthu kuti imuthire nkhondo, mafumu a ku Mediya,+ abwanamkubwa ake, atsogoleri ake onse ndi madera onse olamulidwa ndi aliyense wa amenewa. Danieli 5:28 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 28 “PERESI,* ufumu wanu wagawanika ndipo waperekedwa kwa Amedi ndi Aperisiya.”+ Danieli 8:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 “Nkhosa yamphongo ya nyanga ziwiri imene unaona, ikuimira mfumu ya Mediya ndi mfumu ya Perisiya.+
11 “Nolani mivi yanu.+ Dzitetezeni ndi zishango zozungulira, amuna inu. Yehova wautsa mitima ya mafumu a Amedi,+ chifukwa akufuna kulanga Babulo ndi kumuwononga.+ Yehova akufuna kubwezera Babulo chilango chifukwa cha kachisi wake.+
28 Konzekeretsani mitundu ya anthu kuti imuthire nkhondo, mafumu a ku Mediya,+ abwanamkubwa ake, atsogoleri ake onse ndi madera onse olamulidwa ndi aliyense wa amenewa.