Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 26:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Ndikadzathyola ndodo zanu zopachikapo mkate wozungulira woboola pakati,+ akazi 10 adzaphika mkate mu uvuni umodzi, ndipo adzakugawirani mochita kukuyezerani pamuyezo.+ Chotero mudzadya koma simudzakhuta.+

  • Deuteronomo 28:53
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 53 Pamenepo udzadya chipatso cha mimba yako, mnofu wa ana ako aamuna ndi ana ako aakazi,+ amene Yehova Mulungu wako wakupatsa, chifukwa cha zovuta ndi nsautso zimene adani ako adzakupanikiza nazo.

  • Yesaya 3:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Tamverani! Ambuye woona,+ Yehova wa makamu, akuchotsa mu Yerusalemu+ ndi mu Yuda zinthu zonse zofunika pa moyo. Akuchotsa mkate, madzi,+

  • Ezekieli 4:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Iye anapitiriza kundiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, ine ndidzathyola ndodo mu Yerusalemu. Ndidzathyola ndodo zimene amakolowekapo mikate yozungulira yoboola pakati.+ Anthuwo adzadya chakudya chochita kuyeza ndipo adzachidya ali ndi nkhawa.+ Iwo adzamwa madzi ochita kuyeza ali ndi mantha,+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena