Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mafumu 25:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 M’mwezi wachinayi, pa tsiku la 9,+ njala+ inafika poipa kwambiri mumzindawo, ndipo anthu a m’dzikolo analibiretu chakudya.+

  • Yeremiya 37:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Chotero Mfumu Zedekiya inalamula kuti atsekere Yeremiya m’Bwalo la Alonda+ ndipo anali kumupatsa mtanda wobulungira wa mkate tsiku ndi tsiku. Mkate umenewu unali kuchokera kumsewu wa ophika mkate+ ndipo anapitiriza kum’patsa mkatewo kufikira mkate wonse utatha mumzindamo.+ Choncho Yeremiya anapitiriza kukhala m’Bwalo la Alonda.+

  • Maliro 1:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Anthu ake onse akuusa moyo. Iwo akufunafuna chakudya.+

      Asinthanitsa zinthu zawo zabwino ndi chakudya kuti adzitsitsimutse.+

      Inu Yehova ndiyang’aneni. Onani kuti ndakhala ngati mkazi wachabechabe.+

  • Maliro 4:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  9 Amene anaphedwa ndi lupanga+ aliko bwino kusiyana ndi amene anafa ndi njala,+

      Pakuti amene anafa ndi njala anafooka chifukwa chosowa chakudya, ndipo anakhala ngati apyozedwa ndi lupanga.

  • Maliro 5:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  9 Kuti tipeze chakudya, timaika moyo wathu pachiswe+ chifukwa cha anthu amene ali ndi malupanga m’chipululu.

  • Chivumbulutso 6:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Kenako ndinamva mawu ngati ochokera pakati+ pa zamoyo zinayi zija.+ Mawuwo anali akuti: “Kilogalamu imodzi ya tirigu, mtengo wake ukhala dinari imodzi,+ ndipo makilogalamu atatu a balere, mtengo wake ukhala dinari imodzi. Koma musawononge mafuta a maolivi ndi vinyo.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena