Maliro
5 Inu Yehova, kumbukirani zimene zatichitikira.+ Tiyang’aneni kuti muone chitonzo chathu.+
2 Cholowa chathu chaperekedwa kwa anthu achilendo. Nyumba zathu zaperekedwa kwa alendo.+
3 Ife takhala anthu amasiye opanda bambo.+ Amayi athu akhala ngati akazi amasiye.+
4 Madzi akumwa ndi nkhuni, tikuchita kugula.+
5 Akutithamangitsa ndipo atsala pang’ono kutigwira.+ Tatopa ndipo tikusowa mpumulo.+
6 Kuti tipeze chakudya chokwanira, tikudalira Iguputo+ ndi Asuri.+
7 Makolo athu ndi amene anachimwa.+ Iwo anafa, koma ifeyo ndi amene tikuvutika ndi zolakwa zawozo.+
8 Antchito wamba ndi amene akutilamulira.+ Palibe amene akutilanditsa m’manja mwawo.+
9 Kuti tipeze chakudya, timaika moyo wathu pachiswe+ chifukwa cha anthu amene ali ndi malupanga m’chipululu.
10 Khungu lathu latentha kwambiri ngati ng’anjo, chifukwa cha njala yaikulu.+
11 Achitira zachipongwe+ akazi athu amene ali m’Ziyoni ndi anamwali amene ali m’mizinda ya Yuda.
12 Akalonga athu awapachika dzanja limodzi lokha.+ Anthuwo sanalemekezenso ngakhale amuna okalamba.+
13 Anyamata awanyamulitsa mphero,+ ndipo tianyamata tadzandira polemedwa ndi mitolo ya nkhuni.+
14 Pazipata sipakupezekanso amuna achikulire+ ndipo anyamata sakuimbanso nyimbo ndi zipangizo zawo zoimbira.+
15 Chisangalalo cha mumtima mwathu chatha. Kuvina kwathu kwasanduka kulira maliro.+
16 Chisoti chathu chachifumu chagwa.+ Tsoka kwa ife chifukwa tachimwa!+
17 Pa chifukwa chimenechi, mtima wathu wadwala.+ Chifukwa cha zinthu zimenezi, maso athu achita mdima.+
18 Nkhandwe zayamba kuyendayenda paphiri la Ziyoni chifukwa lasanduka bwinja.+
19 Koma inu Yehova mudzakhala pampando wanu wachifumu mpaka kalekale.+ Mpando wanu wachifumuwo udzakhalapo ku mibadwomibadwo.+
20 N’chifukwa chiyani mwatiiwala kwamuyaya+ ndi kutisiya kwa masiku ambiri?+
21 Inu Yehova, tibwezeni+ kwa inu ndipo ife tibwerera mwamsanga. Mubwezeretse zinthu zonse kuti zikhale ngati mmene zinalili kale.+