Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 26:43
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 43 Pa nthawiyo, adzakhala atasiya dziko lawo, ndipo dzikolo lidzakhala likubweza masabata ake+ pamene lidzakhala bwinja iwowo kulibe. Iwo adzakhala akulipira chifukwa cha zolakwa zawo,+ chifukwa chakuti anakana zigamulo zanga+ ndipo ananyansidwa ndi malamulo anga.+

  • Yeremiya 26:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 “Mika+ wa ku Moreseti+ nayenso anali kunenera m’masiku a Hezekiya mfumu ya Yuda.+ Iye anauza anthu onse a mu Yuda kuti, ‘Yehova wa makamu wanena kuti: “Ziyoni adzagawulidwa ngati munda,+ ndipo Yerusalemu adzangokhala milu ya mabwinja.+ Phiri la nyumba ya Mulungu lidzakhala ngati zitunda za m’nkhalango.”’+

  • Yesaya 32:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Pakuti nsanja yokhalamo yasiyidwa,+ piringupiringu amene anali mumzindamo watha. Ofeli+ ndi nsanja ya mlonda zasanduka tchire. Mpaka kalekale zidzakhala malo osangalalako mbidzi, ndi odyetserako ziweto,

  • Yeremiya 9:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Yerusalemu ndidzamusandutsa milu ya miyala+ ndiponso malo obisalamo mimbulu.+ Mizinda ya Yuda ndidzaisandutsa mabwinja, malo opanda wokhalamo.+

  • Ezekieli 13:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Iwe Isiraeli, aneneri ako akhala ngati nkhandwe za m’mabwinja.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena