2 Mbiri 28:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Pa nthawi imeneyo, Mfumu Ahazi+ inatumiza uthenga kwa mafumu a Asuri+ kuti adzam’thandize. Hoseya 5:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 “Efuraimu anaona kudwala kwake ndipo Yuda anaona chilonda chake.+ Pamenepo Efuraimu anapita ku Asuri+ ndipo anatumiza amithenga kwa mfumu yaikulu.+ Koma mfumuyo sinathe kukuchiritsani anthu inu,+ ndipo sinathe kupoletsa chilonda chanu.+ Hoseya 7:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Efuraimu ali ngati nkhunda yopusa,+ yopanda nzeru.+ Iwo apempha thandizo ku Iguputo+ ndiponso apita kudziko la Asuri.+ Hoseya 9:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Iwe sudzapitiriza kukhala m’dziko la Yehova.+ Efuraimu adzabwerera ku Iguputo+ ndipo adzadya zinthu zodetsedwa kudziko la Asuri.+ Hoseya 12:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 “Efuraimu akudya mphepo+ ndi kuthamangitsa mphepo ya kum’mawa tsiku lonse.+ Iye akuchulukitsa mabodza ndipo akuwononga zinthu zambiri.+ Wachita pangano ndi Asuri+ ndipo wapititsa mafuta ku Iguputo.
13 “Efuraimu anaona kudwala kwake ndipo Yuda anaona chilonda chake.+ Pamenepo Efuraimu anapita ku Asuri+ ndipo anatumiza amithenga kwa mfumu yaikulu.+ Koma mfumuyo sinathe kukuchiritsani anthu inu,+ ndipo sinathe kupoletsa chilonda chanu.+
11 Efuraimu ali ngati nkhunda yopusa,+ yopanda nzeru.+ Iwo apempha thandizo ku Iguputo+ ndiponso apita kudziko la Asuri.+
3 Iwe sudzapitiriza kukhala m’dziko la Yehova.+ Efuraimu adzabwerera ku Iguputo+ ndipo adzadya zinthu zodetsedwa kudziko la Asuri.+
12 “Efuraimu akudya mphepo+ ndi kuthamangitsa mphepo ya kum’mawa tsiku lonse.+ Iye akuchulukitsa mabodza ndipo akuwononga zinthu zambiri.+ Wachita pangano ndi Asuri+ ndipo wapititsa mafuta ku Iguputo.