Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yeremiya 37:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Chotero Mfumu Zedekiya inalamula kuti atsekere Yeremiya m’Bwalo la Alonda+ ndipo anali kumupatsa mtanda wobulungira wa mkate tsiku ndi tsiku. Mkate umenewu unali kuchokera kumsewu wa ophika mkate+ ndipo anapitiriza kum’patsa mkatewo kufikira mkate wonse utatha mumzindamo.+ Choncho Yeremiya anapitiriza kukhala m’Bwalo la Alonda.+

  • Yeremiya 38:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 “Yehova wanena kuti, ‘Amene adzapitirize kukhala mumzinda uno adzafa ndi lupanga,+ njala yaikulu+ kapena mliri.+ Koma amene adzadzipereke kwa Akasidi adzakhala ndi moyo. Adzapulumutsa moyo wake, sadzafa ayi.’+

  • Maliro 4:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Lilime la ana oyamwa lamamatira kummero chifukwa cha ludzu.+

      Ana apempha chakudya+ koma palibe amene akuwapatsa.+

  • Ezekieli 5:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Gawo limodzi la magawo atatu a anthu a mtundu wako adzafa ndi mliri+ ndipo adzatha ndi njala pakati pako.+ Gawo lina la magawo atatu a anthu a mtundu wako adzaphedwa ndi lupanga mokuzungulira. Gawo lomaliza la magawo atatu a anthu a mtundu wako ndidzawabalalitsira kumphepo zonse zinayi,+ ndipo ndidzawatsatira nditasolola lupanga.+

  • Ezekieli 7:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Lupanga+ lili panja ndipo mliri ndi njala zili mkati.+ Yemwe ali kutchire adzaphedwa ndi lupanga, ndipo amene ali mumzinda njala ndi mliri zidzawasakaza.+

  • Ezekieli 14:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 “Chotero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Zidzateronso ndikadzabweretsa ziweruzo zanga zinayi izi zowononga:+ lupanga, njala, zilombo zolusa zakutchire ndi mliri.+ Ndidzatumiza zimenezi mu Yerusalemu kuti zikaphemo anthu ndi ziweto.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena