Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yobu 34:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Iye akachititsa bata, ndani angamudzudzule?

      Ndipo akabisa nkhope yake,+ ndani angamuone?

      Kaya abisire nkhope yake mtundu+ kapena munthu, n’chimodzimodzi.

  • Salimo 34:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Nkhope ya Yehova imakwiyira anthu ochita zoipa,+

      Kuti dzina lawo lisatchulidwenso padziko lapansi.+

  • Yesaya 59:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Ayi si choncho. Koma zolakwa za anthu inu n’zimene zakulekanitsani ndi Mulungu wanu,+ ndipo machimo anu amuchititsa kuti akubisireni nkhope yake, kuti asamve zimene mukunena.+

  • Yeremiya 18:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Ndidzawamwaza pamaso pa adani awo ngati mmene mphepo yochokera kum’mawa imamwazira fumbi.+ Sindidzawaonetsa nkhope yanga,+ koma ndidzawafulatira pa tsiku la tsoka lawo.”

  • Aheberi 8:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 ‘Koma pangano+ limeneli si lofanana ndi limene ndinapangana ndi makolo awo pamene ndinagwira dzanja lawo kuti ndiwatulutse m’dziko la Iguputo,+ chifukwa iwo sanapitirize kusunga pangano+ langalo moti ndinasiya kuwasamalira,’ watero Yehova.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena