5 Pamenepo gulu lankhondo la Akasidi linawathamangitsa+ ndipo Zedekiya anamupeza m’chipululu cha Yeriko.+ Atamugwira, anamutenga ndi kupita naye kwa Nebukadirezara mfumu ya Babulo ku Ribila,+ m’dziko la Hamati,+ kuti Nebukadirezara akamuweruze.+
13 Ine ndidzamutambasulira ukonde wanga. Chotero iye adzakodwa mu ukonde wanga wosakira+ ndipo ndidzamupititsa ku Babulo, kudziko la Akasidi.+ Koma iye sadzaliona ndipo adzafera komweko.+