Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mafumu 25:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Gulu lankhondo la Akasidi+ linayamba kuthamangitsa mfumuyo ndipo linaipeza+ m’chipululu cha Yeriko.+ Pamenepo gulu lonse lankhondo la mfumuyo linabalalika n’kuisiya yokha.

  • Yeremiya 24:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 “‘Chotero mofanana ndi nkhuyu zoipa zija zimene munthu sangadye chifukwa cha kuipa kwake,+ Yehova wanena kuti: “Momwemonso ndidzapereka Zedekiya+ mfumu ya Yuda, akalonga ake ndi anthu onse opulumuka mu Yerusalemu amene atsalira m’dzikoli,+ komanso anthu okhala m’dziko la Iguputo.+

  • Yeremiya 34:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Ndipo Zedekiya mfumu ya Yuda+ ndi akalonga ake ndidzawapereka m’manja mwa adani awo, m’manja mwa anthu ofuna moyo wawo ndiponso m’manja mwa magulu ankhondo a mfumu ya ku Babulo+ amene akubwerera osakuthirani nkhondo.’+

  • Yeremiya 37:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Kenako Mfumu Zedekiya inatuma anthu kuti akatenge Yeremiya. Atabwera naye, mfumuyo inayamba kumufunsa mafunso m’nyumba mwake pamalo obisika.+ Mfumuyo inamufunsa kuti: “Kodi pali mawu aliwonse ochokera kwa Yehova?” Pamenepo Yeremiya anayankha kuti: “Inde alipo!” Ndiyeno Yeremiya ananenanso kuti: “Inuyo mudzaperekedwa m’manja mwa mfumu ya Babulo!”+

  • Yeremiya 38:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Koma ngati simudzadzipereka kwa akalonga a mfumu ya Babulo, ndiye kuti mzinda uno udzaperekedwa m’manja mwa Akasidi ndipo adzautentha.+ Inuyo simudzapulumuka m’manja mwawo.’”+

  • Yeremiya 39:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Pamenepo gulu lankhondo la Akasidi linawathamangitsa+ ndipo Zedekiya anamupeza m’chipululu cha Yeriko.+ Atamugwira, anamutenga ndi kupita naye kwa Nebukadirezara mfumu ya Babulo ku Ribila,+ m’dziko la Hamati,+ kuti Nebukadirezara akamuweruze.+

  • Ezekieli 12:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Ine ndidzamutambasulira ukonde wanga. Chotero iye adzakodwa mu ukonde wanga wosakira+ ndipo ndidzamupititsa ku Babulo, kudziko la Akasidi.+ Koma iye sadzaliona ndipo adzafera komweko.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena