2 Tsopano Yehova anayamba kum’tumizira Yehoyakimu magulu a achifwamba a Akasidi,+ a Asiriya, a Amowabu,+ ndi a ana a Amoni. Ankawatumiza ku Yuda kuti awononge dzikolo mogwirizana ndi mawu a Yehova+ amene analankhula kudzera mwa atumiki ake, aneneri.
25M’chaka cha 9+ cha ufumu wa Zedekiya, m’mwezi wa 10,+ pa tsiku la 10 la mweziwo, Nebukadinezara+ mfumu ya Babulo anabwera+ ku Yerusalemu pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo. Anabwera kudzachita nkhondo ndi mzindawo ndipo anamanga misasa ndi khoma kuzungulira mzinda wonsewo.+