14 Pakuti nsanja yokhalamo yasiyidwa,+ piringupiringu amene anali mumzindamo watha. Ofeli+ ndi nsanja ya mlonda zasanduka tchire. Mpaka kalekale zidzakhala malo osangalalako mbidzi, ndi odyetserako ziweto,
12 Chotero Ziyoni adzagawulidwa ngati munda chifukwa cha anthu inu ndipo Yerusalemu adzangokhala milu ya mabwinja.+ Phiri la nyumba ya Mulungu lidzakhala ngati zitunda za m’nkhalango.