7 Wowonongayo akubwera ngati mkango umene ukutuluka paziyangoyango pamene umakhala.+ Amene akuwononga mitundu ya anthu wanyamuka.+ Wachoka m’malo ake kuti adzasandutse dziko lanu chinthu chodabwitsa. Mizinda yanu idzagwa ndi kukhala mabwinja moti sipadzapezeka wokhalamo.+