16 Aroni ndi ana ake azidya zotsala za nsembe imeneyi.+ Azipanga mkate wopanda chofufumitsa+ ndi kudya mkatewo m’malo oyera. Aziudyera m’bwalo la chihema chokumanako.
13 Mudye nsembeyo m’malo oyera,+ chifukwa ndi gawo lanu komanso ndi gawo la ana anu kuchokera pa nsembe zotentha ndi moto zoperekedwa kwa Yehova. Zimenezi n’zimene ndalamulidwa.
9 Mkatewo uzikhala wa Aroni ndi ana ake,+ ndipo aziudyera m’malo oyera,+ chifukwa wapatsidwa kwa iye monga chinthu choyera koposa kuchokera pa nsembe zotentha ndi moto zoperekedwa kwa Yehova. Limeneli likhale lamulo mpaka kalekale.”