7 Panali pa nthawi imeneyi pamene Solomo anamangira Kemosi+ malo okwezeka,+ chinthu chonyansa+ cha Mowabu, paphiri+ lomwe linali patsogolo+ pa Yerusalemu. Anamangiranso Moleki malo okwezeka, yemwe ndi chinthu chonyansa cha ana a Amoni.
7 Komanso iye anaika m’nyumba ya Mulungu woona+ chifaniziro+ chimene anapanga. Koma ponena za nyumba imeneyo, Mulungu anauza Davide ndi Solomo mwana wake kuti: “M’nyumba iyi ndiponso mu Yerusalemu mzinda umene ndausankha+ pa mafuko onse a Isiraeli, ndidzaikamo dzina langa+ mpaka kalekale.+