Ezekieli 39:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Ndidzachititsa kuti dzina langa loyera lidziwike pakati pa anthu anga Aisiraeli. Sindidzalolanso kuti dzina langa lidetsedwe,+ ndipo mitundu ina ya anthu idzadziwa kuti ine ndine Yehova,+ Woyera wa ku Isiraeli.’+ Hoseya 14:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 “Efuraimu adzanena kuti, ‘Kodi mafano ndi a chiyaninso kwa ine?’+ “Ine ndidzamva ndipo ndidzapitirizabe kumuyang’anira.+ Ine ndili ngati mtengo waukulu wa mkungudza wamasamba obiriwira+ ndipo mudzapeza zipatso kwa ine.” Zekariya 13:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Yehova wa makamu wanena kuti, “Pa tsiku limenelo, ndidzathetsa mayina a mafano m’dziko lonseli+ ndipo mafanowo sadzakumbukiridwanso. M’dzikoli ndidzachotsamo aneneri+ komanso mzimu wonyansa.+
7 Ndidzachititsa kuti dzina langa loyera lidziwike pakati pa anthu anga Aisiraeli. Sindidzalolanso kuti dzina langa lidetsedwe,+ ndipo mitundu ina ya anthu idzadziwa kuti ine ndine Yehova,+ Woyera wa ku Isiraeli.’+
8 “Efuraimu adzanena kuti, ‘Kodi mafano ndi a chiyaninso kwa ine?’+ “Ine ndidzamva ndipo ndidzapitirizabe kumuyang’anira.+ Ine ndili ngati mtengo waukulu wa mkungudza wamasamba obiriwira+ ndipo mudzapeza zipatso kwa ine.”
2 Yehova wa makamu wanena kuti, “Pa tsiku limenelo, ndidzathetsa mayina a mafano m’dziko lonseli+ ndipo mafanowo sadzakumbukiridwanso. M’dzikoli ndidzachotsamo aneneri+ komanso mzimu wonyansa.+