Levitiko 19:36 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 36 Muzikhala ndi masikelo olondola,+ miyala yolondola yoyezera kulemera kwa zinthu, muyezo wolondola wa efa ndi muyezo wolondola wa hini.* Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani m’dziko la Iguputo. Miyambo 11:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Sikelo yachinyengo imam’nyansa Yehova,+ koma mwala woyezera, wolemera mokwanira, umam’sangalatsa. Miyambo 16:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Muyezo wachilungamo ndiponso masikelo ndi za Yehova.+ Miyala yonse ya m’thumba loyezera kulemera kwa zinthu ndiyo ntchito zake.+ Miyambo 20:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Miyezo iwiri yosiyana yoyezera kulemera kwa chinthu ndiponso miyezo iwiri yosiyana ya efa,*+ zonsezi n’zonyansa kwa Yehova.+ Amosi 8:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Inu mukunena kuti: ‘Kodi mwezi watsopano utha liti+ kuti tiyambe kugulitsa chakudya?*+ Komanso sabata+ litha liti kuti tiyambe kuchepetsa muyezo wogulitsira zinthu,+ kukweza mtengo ndi kubera wogula mwa kugwiritsa ntchito masikelo achinyengo?+ Mika 6:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Kodi ndingakhale woyera ndili ndi sikelo yachinyengo, ndiponso thumba lachinyengo lamiyala yoyezera zinthu?+
36 Muzikhala ndi masikelo olondola,+ miyala yolondola yoyezera kulemera kwa zinthu, muyezo wolondola wa efa ndi muyezo wolondola wa hini.* Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani m’dziko la Iguputo.
11 Muyezo wachilungamo ndiponso masikelo ndi za Yehova.+ Miyala yonse ya m’thumba loyezera kulemera kwa zinthu ndiyo ntchito zake.+
10 Miyezo iwiri yosiyana yoyezera kulemera kwa chinthu ndiponso miyezo iwiri yosiyana ya efa,*+ zonsezi n’zonyansa kwa Yehova.+
5 Inu mukunena kuti: ‘Kodi mwezi watsopano utha liti+ kuti tiyambe kugulitsa chakudya?*+ Komanso sabata+ litha liti kuti tiyambe kuchepetsa muyezo wogulitsira zinthu,+ kukweza mtengo ndi kubera wogula mwa kugwiritsa ntchito masikelo achinyengo?+
11 Kodi ndingakhale woyera ndili ndi sikelo yachinyengo, ndiponso thumba lachinyengo lamiyala yoyezera zinthu?+