-
Levitiko 14:21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 “Koma ngati munthuyo ali wosauka+ ndipo sangakwanitse kupeza zinthu zimenezi,+ azibweretsa nkhosa yaing’ono yamphongo imodzi monga nsembe ya kupalamula. Nsembeyo aziiweyulira uku ndi uku kuti am’phimbire machimo. Azibweretsanso muyezo umodzi wa mafuta ndi ufa wosalala wothira mafuta. Ufawo uzikhala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa, monga nsembe yake yambewu.
-
-
Ezekieli 46:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Pa nthawi ya zikondwerero+ ndi pa nyengo ya zikondwerero zanu, azipereka ng’ombe yaing’ono yamphongo pamodzi ndi nsembe yambewu yokwana muyezo wa efa. Aziperekanso nkhosa yamphongo pamodzi ndi nsembe yambewu yokwana muyezo wa efa. Popereka ana a nkhosa amphongo aziperekanso nsembe yambewu imene angakwanitse. Pa nsembe iliyonse yambewu yokwana muyezo wa efa azipereka mafuta okwana muyezo wa hini.+
-