15 “‘Ansembe achilevi,+ ana a Zadoki,+ amene anali kugwira ntchito za pamalo anga opatulika pamene ana a Isiraeli anachoka kwa ine n’kupita kutali,+ amenewa adzandiyandikira ndi kunditumikira. Iwo adzaima pamaso panga+ ndi kundipatsa mafuta+ ndi magazi,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.