30 “‘Chotero ine ndidzaweruza aliyense wa inu malinga ndi njira zake,+ inu a nyumba ya Isiraeli,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.+ ‘Lapani ndi kusiya zolakwa zanu zonse+ ndipo musalole kuti chilichonse chizikupunthwitsani ndi kukulakwitsani.+
20 “Anthu inu mwanena kuti, ‘Njira za Yehova n’zopanda chilungamo.’+ Inu a nyumba ya Isiraeli, ine ndidzaweruza aliyense wa inu malinga ndi njira zake.”+