23 Pamenepo Yehova akamapita kukapha Aiguputo ndi mliri, akaona magazi pamafelemu a pamwamba pa zitseko zanu ndi mafelemu awiri a m’mbali mwa khomo, Yehova adzapitirira khomo limenelo ndipo sadzalola chiwonongeko kulowa m’nyumba zanu ndi kukuphani.+
18 Tikubwera ndithu m’dziko muno! Chingwe chofiira ichi uchimangirire pawindo limene watitulutsirapo. Bambo ako ndi mayi ako, abale ako ndi alongo ako, ndi onse a m’nyumba ya bambo ako, uwasonkhanitse kuti adzakhale m’nyumba mwako.+