10 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pa chifukwa chimenechi ine ndilanga abusawo.+ Ndiwauza kuti andibwezere nkhosa zanga ndipo ndiwaletsa kudyetsa nkhosa zangazo.+ Abusawo sadzadzidyetsanso okha.+ Ndidzalanditsa nkhosa zanga kukamwa kwawo ndipo sizidzakhalanso chakudya chawo.’”+