2 Mafumu 17:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Koma iwo sanamvere. M’malomwake anaumitsa makosi awo,+ ngati mmene makolo awo anaumitsira makosi awo. Makolo awowo sanasonyeze chikhulupiriro+ mwa Yehova Mulungu wawo. 2 Mbiri 36:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Koma iwo ankangonyogodola+ amithenga a Mulungu woona, kunyoza mawu ake+ ndi kuseka+ aneneri ake, mpaka kufika poti panalibenso chiyembekezo choti angathe kuchiritsidwa.+ Kenako mkwiyo+ wa Yehova unawagwera. Yeremiya 7:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Tsopano chifukwa chakuti mwapitiriza kuchita ntchito zimenezi,’ watero Yehova, ‘ndipo ndinali kukulankhulani nthawi zonse, kudzuka m’mamawa ndi kukulankhulani,+ koma inu osamva,+ kukuitanani koma inu osandiyankha,+ Yeremiya 29:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 Ndidzawachitira zimenezi chifukwa chakuti sanamvere mawu anga amene ndinali kuwatumizira kudzera mwa atumiki anga aneneri. Ndinali kudzuka m’mawa kwambiri ndi kutumiza atumiki angawo,’+ watero Yehova. “‘Inunso simunandimvere,’+ watero Yehova. Yeremiya 44:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Koma inu simunamvere+ kapena kutchera khutu lanu kuti musiye kuchita zinthu zoipa zomwe ndi kupereka nsembe zautsi kwa milungu ina.+
14 Koma iwo sanamvere. M’malomwake anaumitsa makosi awo,+ ngati mmene makolo awo anaumitsira makosi awo. Makolo awowo sanasonyeze chikhulupiriro+ mwa Yehova Mulungu wawo.
16 Koma iwo ankangonyogodola+ amithenga a Mulungu woona, kunyoza mawu ake+ ndi kuseka+ aneneri ake, mpaka kufika poti panalibenso chiyembekezo choti angathe kuchiritsidwa.+ Kenako mkwiyo+ wa Yehova unawagwera.
13 Tsopano chifukwa chakuti mwapitiriza kuchita ntchito zimenezi,’ watero Yehova, ‘ndipo ndinali kukulankhulani nthawi zonse, kudzuka m’mamawa ndi kukulankhulani,+ koma inu osamva,+ kukuitanani koma inu osandiyankha,+
19 Ndidzawachitira zimenezi chifukwa chakuti sanamvere mawu anga amene ndinali kuwatumizira kudzera mwa atumiki anga aneneri. Ndinali kudzuka m’mawa kwambiri ndi kutumiza atumiki angawo,’+ watero Yehova. “‘Inunso simunandimvere,’+ watero Yehova.
5 Koma inu simunamvere+ kapena kutchera khutu lanu kuti musiye kuchita zinthu zoipa zomwe ndi kupereka nsembe zautsi kwa milungu ina.+