Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mbiri 36:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Koma iwo ankangonyogodola+ amithenga a Mulungu woona, kunyoza mawu ake+ ndi kuseka+ aneneri ake, mpaka kufika poti panalibenso chiyembekezo choti angathe kuchiritsidwa.+ Kenako mkwiyo+ wa Yehova unawagwera.

  • Nehemiya 9:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Ngakhale kuti munali kuwalimbikitsa+ kuti abwerere ku chilamulo chanu,+ iwo anali kuchita zinthu modzikuza+ ndipo sanali kumva malamulo anu. Anachimwira zigamulo zanu,+ zimene ngati munthu azitsatira adzakhala ndi moyo chifukwa cha zigamulozo.+ Iwo anatseka makutu*+ awo ndi kuumitsa khosi+ lawo ndipo sanamvere.+

  • Yeremiya 11:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Koma iwo sanamvere kapena kutchera khutu.+ M’malomwake aliyense wa iwo anapitiriza kuumitsa mtima wake woipawo.+ Choncho ndinawalanga mogwirizana ndi mawu onse amene ndinanena m’pangano langa, amene ndinawalamula kuti awasunge, koma sanawasunge.’”

  • Yeremiya 25:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 “Kuyambira m’chaka cha 13 cha ulamuliro wa Yosiya+ mwana wa Amoni, mfumu ya Yuda, kufikira lero, zaka 23 zonsezi, Yehova wakhala akundiuza mawu ndipo ine ndakhala ndikukuuzani mawuwo, kudzuka m’mawa kwambiri ndi kukuuzani mawu akewo koma simunandimvere.+

  • Zekariya 1:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 “‘Musakhale ngati makolo anu+ amene aneneri akale anawauza mofuula+ kuti: “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Chonde, siyani njira zanu zoipa ndi zochita zanu zoipa n’kubwerera kwa ine!’”’+

      “‘Koma iwo sanamvere ndipo sanalabadire mawu anga,’+ watero Yehova.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena