Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Nehemiya 9:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 “Koma iwo, makolo athu, anachita zinthu modzikuza+ moti anaumitsa khosi lawo+ ndipo sanamvere malamulo anu.

  • Yeremiya 6:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Yehova wauza anthuwo kuti: “Imani chilili panjira anthu inu, kuti muone ndi kufunsa za njira zakale, kuti mudziwe kumene kuli njira yabwino.+ Mukaipeza muyende mmenemo+ kuti mupeze mpumulo wa miyoyo yanu.”+ Koma iwo anapitiriza kunena kuti: “Ife sitiyendamo.”+

  • Yeremiya 7:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Koma iwo sanandimvere kapena kutchera khutu lawo.+ M’malomwake anapitiriza kuumitsa khosi lawo,+ ndipo anachita zinthu zoipa kuposa makolo awo.+

  • Ezekieli 20:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 “‘“Koma iwo anayamba kundipandukira+ ndipo sanafune kundimvera. Aliyense wa iwo sanataye zinthu zonyansa zimene anali kuziyang’anitsitsa pozilambira ndipo sanasiye mafano onyansa a ku Iguputo.+ Choncho ine ndinatsimikiza mtima kuwatsanulira mkwiyo wanga kuti ukali wanga uthere pa iwo m’dziko la Iguputo.+

  • Zekariya 7:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Koma iwo anakanabe kumvetsera.+ Anapitiriza kumulozetsa nkhongo+ ndipo anatseka makutu awo kuti asamve chilichonse.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena