-
Danieli 4:19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 “Pa nthawi imeneyo Danieli, wotchedwa Belitesazara,+ anada nkhawa kwa kanthawi ndipo anachita mantha.+
“Chotero mfumuyo inamuuza kuti, ‘Iwe Belitesazara, malotowa ndi kumasulira kwake zisakuchititse mantha.’+
“Belitesazara anayankha kuti, ‘Inu mbuyanga, zikanakhala bwino malotowa akanakhala okhudza anthu amene amadana nanu. Zikanakhalanso bwino kumasulira kwake kukanakhala kokhudza adani anu.+
-
-
Danieli 5:12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Anachita zimenezi chifukwa munthuyu anali ndi luso lodabwitsa, anali wodziwa zinthu ndi wozindikira pa nkhani yomasulira maloto,+ kumasulira mikuluwiko ndi kumasula mfundo. Zinthu zonsezi zinapezeka mwa munthu ameneyu+ Danieli, amene mfumu inamupatsa dzina lakuti Belitesazara.+ Tsopano itanani Danieli kuti adzakuuzeni kumasulira kwa zolembedwazi.”
-