Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Numeri 11:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Ine nditsikira kumeneko+ kudzalankhula nawe.+ Ndidzatengako gawo lina la mzimu+ umene uli pa iwe n’kuuika pa iwo. Pamenepo iwo adzatha kukuthandiza kusenza udindo woyang’anira anthuwo, kuti usausenze wekhawekha.+

  • Yesaya 63:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Iwo anayamba kukumbukira masiku akale, masiku a Mose mtumiki wake, ndipo anafunsa kuti: “Kodi amene anawatulutsa m’nyanja+ pamodzi ndi abusa a anthu ake uja, ali kuti?+ Ali kuti amene anaika mzimu wake woyera mwa iye?+

  • Danieli 4:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 “‘Amenewa ndiwo maloto amene ine Mfumu Nebukadinezara ndinalota. Tsopano iwe Belitesazara umasulire malotowa, pakuti amuna ena onse anzeru a mu ufumu wanga alephera kuwamasulira.+ Koma iwe ungathe kuwamasulira chifukwa mzimu wa milungu yoyera uli mwa iwe.’+

  • Danieli 4:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 lamulo+ la Wam’mwambamwamba+ ligwera inu mbuyanga mfumu,+ ndipo kumasulira kwake ndi uku:

  • Danieli 5:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Mu ufumu wanu muli munthu amene ali ndi mzimu wa milungu yoyera.+ M’masiku a bambo anu, anthu anazindikira kuti munthuyu ndi wodziwa zinthu kwambiri, wozindikira ndiponso ali ndi nzeru zofanana ndi nzeru za milungu. Chotero bambo anu, Mfumu Nebukadinezara, anamuika kukhala mkulu+ wa ansembe ochita zamatsenga, anthu okhulupirira mizimu, Akasidi ndi anthu okhulupirira nyenyezi. Ndithudi mfumu, bambo anu anamupatsa udindo umenewu.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena